| Chichewa | Malankhulidwe ena |
| Kodi
Mwalandira Yesu Kodi mudziwa bwanji kuti yesu alowa zoona? Mudziwa popeza ambuye Yesu analonjeza kuti adzalowa pamene mutsegula pa khomo ndikumuuza kuti alowe. Ngati mwapemphera ndi mtima woona, khulupirirani kuti Yesu alowa monga analonjeza. Mau a Mulungu
Aalonjeza Moyo
Wosatha Yamikani Mulungu tsiku ndi tsiku cifukwa mwalandira Yesu Kristu
ndiponso kuti iye anakupatsani moyo wosatha. Yesu analonjeza kuti
sadzakusiyani. Otsaiwala ai... Khulupirani Mulungu,
Zina
Zibwela M'mbyo
Pamene Mwalandira Yesu Kristu... Pamene mulandira Yesu Kristu mwa cikhulupiriro, izi zicitika mu m'moyo wanu:
Kodi pali dalitso lina loposa ili lomwe mukhoza kuzindikira kuti muli
ndi moyo wosatha cifukwa Yesu Kristu anakuferani ndi kukupulumutsani? Tsopano ticita ciani? Tsopano Muyenera
Kukula
Nkuni itakhala pa yokho, moto suyaka bwino. Pafunika kuti ikhale ndi zinzace kuti moto uyake bwino. Motero inunso simungathe kukhala ndi moyo weni-weni wabwino panokha osayanjana ndi Akristu anzanu. Muyenera kulowa mu mpingo kuti muyanjane ndi Akristu anzanu omwe analandira Mau a Mulungu. Zina zomuthandizani kukula mu Cikristi. Ngati mufuna kumva zina za moyo wa Cikristu ndi m'mene mungathe kuphunzira zina, tumani fomu, kapena lembani kalata ku Campus Crusade for Christ-Zambia P.O. Box 36176 Lusaka, Zambia, ndiponso mungathe kutuma formu iyi. Kodi mau awa amuthandizani? Ngati zimene mwawerenga lelo zakuthanzizani gawani kwa Munthu wina. In order to maintain the quality and protect the contents from changes, neither this page nor parts thereof (including mirror sites) may be reproduced in any form without written permission from the publisher, NewLife Publications, P.O. Box 593684, Orlando, FL 32859. The Four Spiritual Laws was written by Dr. Bill
Bright |
© 2002 Campus Crusade for Christ International
Last Updated: 14 March, 2002