|
M'buku la Mau a Mulungu tiwerenga za anthu
a mitundu itatu:
1. Munthu Amene Sanamulandile Yesu
Kristu M'moyo Wace.
"Munthu amene alibe Mzimu
Woyera, amakana zimene zili za Mzimu wa Mulungu. Amaziyesa zopusa,
ndipo sngathe kudziwa, popeza kuti munthu amazindikira pokhapokha atakhala
ndi Mzimu Woyera" (1 Akorinto 2:14).
 |
MUNTHU AMENE SALI MKRISTU. INE ndiri pa mpando.
Munthu mwini wake amalamulira zonse za moyo wake.
Zamoyo zace zonse zasokonezeka.
YESU ali pabwalo, salandiridwa. |
2. Mkristu wodzala ndi Mzimu Woyera.
"Koma chipatsi cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza
mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso, pokana
zimenezi palibe lamulo (Agalatiya 5;22'23).
 |
MKRISTU ODZALA NDI MZIMU OYERA YESU
ndiye mfumu ndipo alamulira za m'moyo wange.
INE ndibvomela ndi kutumikira Yesu.
Zamoyo zanga zonse zalongosoka. |
3. Mkristu Wodzilamulira yekha.
"Ndipo ine abale, sidinakhoza
kulankhula ndi inu monga ndi auzimu, koma monga athupi, monga makanda mwa
Kristu. Ndnadyetsa inu mkaka, sichakudya cholimba ayi; pakuti
simunachikhoza; pakuti mulino athupi; pakuti pokhala pali nkhwidzi ndi
ndeu pakati pa inu, simuli a thupi kodi? Ndikuyendayenda monga mwa
munthu?"
(1 Akorinto 3:1-3).
 |
MKRISTU WODZILAMULIRA YEKHA INE
ndiri pa mpando
Yesu acotsedwa pa mpando. Sasogolela moyo wanga.
Za moyo zanga zisokonezeka |
| 1.
Mulungu atipasta ife moyo ocuruka ndiponso wa zipatso mu Cikritu. |
- "Koma cipatso ca uzimu ndico cikondi, cimwemwe,mtendere,
kuleza mtima, cifundo, kikoma mtima, cikhulupiriro, cifatso, ciletso:
pokana zimenezi palibe lamulo" (Agalatiya
5:22, 23).
- "Komatu mudzalandira mphavu, Mzimu Woyera atadza pa inu:
ndipo mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi
m'Samariya, ndi kufikira malekezero ace a dziko"(Macitidwe 1:8).
Mkristu wodzala ndi Mzimu Woyera
Amalola Yesu kukhala pa mpando, ali ndi mphamvu
yopatsidwa ndi Mzimu Woyera wokhala mwa iye.
Amafitsa anthu ena kwa Yesu
Amapemphera mwa chikhulupiriro |
 |
Chikondi
Chimwemwe
Mtendere
Kukoma-mtima
Kukhulupilira
Kuleza mtima
Cifatso
Ciletso
|
Ngati Mkristu akhala ozipereka kwa Mulungu Atate tsiku ndi tsiku muz
adzakhala wakukula mucikristu chace.
Kodi ndi cifukwa ciani anthu ambirir amasowa moyo weni-weni wabino?
| 2.
Mkristu wodzilamulira Yekha. |
Mkristu wodzilamulira amangofuna kudzikonweretsa yekha
nthawi zonse, osati kukonweletsa Mulungu.
- Ameneyo saziwa kapena aiwala za chikondi ndi kukuhulukidwa ndi mpamvu
za Ambuye Yesu. (Aroma 5:8-10; Ahebri 11:2; I John 1:1-3; 2
Petro 1:9; Macitidwe 1:8).
- Kawirikawiri amagonjera zoipa ndikulephera kukhala mkristu wa moyo
woculuka.
- Mwina afunitsitsa kukondweretsa Mulungu koma amalephera.
- Salola Mzimu Oyera ku umupatse mphamvu.
(1 Akorinto 3:1-3; Aroma 7:15-24; 8:7; Agalatiya 5:16-18)
Mkristu wodzilamulira yekha- Chithunzi ichi chifanizira munthu
wodzilamulira yekha:
Mkristuyu...
Sakhulupirira Mulungu ndi mtima wake onse
Amakhala osanvera Mulungu
Sadandaulila ena kuti alandire Yesu
Mtima wace sugundira kupemphera |
 |
Maganizo Oipa
Nsanje
Nkhawa
Kuptsa mtima
Kuweruza ena
Kukhumudwa
Kuda nkhawa
Kufoka mtima
Kukhumudwa
|
(Munthu amene alankhula kuti ndi Mkristu koma umoyo wace suonetsa
zipatso za Uzimu, m'eneyo si Mkristu ayi . Tiyeni tione
momwe tingathe kulandirila Yesu).
Coona Ca Citatu Citionetsa Njira...
| 3.
Yesu alonjeza moyo ocuruka ndipo wa zipatso cifukwa co dzazidwa ndi
Mzimu Woyera. |
Kusogoleledwa ndi Mzimu Woyera
ndi kustsogoleredwa ndi Yesu Kristu, ndipo Yesu atipatsa mphavu zogonjetsa
zoipa(Yohane 15).
- Ife tasandulika kuti tikhale akristu
pokhulupilira Yesu Kristu kuti ndiye Mpulumutsi wathu.
Tisandulikanso akristu wodzala ndi Mzimu Woyera mwa kukhulupirira.
Ngakhale
ali ndi Mzimu Woyera, sionse amene atsogoleledwa ndi Mzimu Woyera.
- Mzimu Woyera utipatsa moyo ocuruka
(Yohane7:37-39).
- Mzimu Woyera unadza ku pereka ulemelelo kwa Yesu
Kristu. Pamene tidzazidwa ndi Mzimu Woyera, tikhala ophunzira
eni-eni a Yesu Kristu.
- Mu lamulo yakhe yosiliza pamene sanaunkhe kwa
Atete ace, Yesu analonjeza Kutuma Mzimu Oyera kuti ife ticile umboni
oona (Macitidwe1:1-9).
Kodi ndigalandile bwaji Mzimu Oyera?
| 4. Ife
tasandulika kuti tikhale akristu pokhulupilira Yesu Kristu kuti ndiye
Mpulumutsi wathu. Tisandulikanso akristu wodzala ndi Mzimu
Woyera mwa kukhulupirira.
. |
Mungathe kupempha tsopano kuti Mzimu
Woyera adzaze ndi kulamulira moyo wanu:
- Funitsitsani kutsogololedwa ndi Mzimu Oyera. (Mateyo
5:6; Yohane 7:37-39).
- Lapani machimo anu. Mwacikhulupiliro dziwani kuti
Mulungu akhululikila macimo anu onse cifukwa Yesu Kristu anakufereni za
kwaipa zanu zonse (Akolose 2:13-15; 1 Yohane 1; 2:1-3; Aheberi 10:1-17).
- Dziperekeni kwathunthu kwa Mulungu (Aroma 12:1,2).
- Khulupilirani kuti Mulungu adzachita:
1. Ndi Lamulo - Mulungu
alamula kuti tidzazidwe, "Ndipo musaledzere nayo vinyo, m'mene
muli chitayiko; koma mudzale naye Mzimu (Aefenso 5:18).
2. Ndi Lonjezo - Mulungu
alonjeza kuti adzatimvera. "Ndipo uku ndi kulimba mtima kumene
tili nako kwa iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro
chake, atinvera; ndipo ngati tidziwa kuti atinvera chilichonse
tichipemph, tidziwa kutitilinazo izi tazipempha kwa iye." (1
Yohane 5:14, 15).
Mwacikulupiriro munkhathe kupemphera...
Mungathe
Kudzazidwa ndi Mzimu Woyera Tsopano
Tilandila Mzimu Woyera pamene tipemphera mwacikulupiriro.
Pempherani ndipo khululupirani kuti mulndira Mzimu Woyera.
"Ambuye Yesu, ndivomera kuti ndakhala ndili kulamulira
moyo wang ndeka. Ndazindikira kuti mwakutero ndiri kuchimwira
inu. Tsopano ndaleka njira iyi. Ndifuna kuti inu
mulamulire myo wanga wonse. motero ndidzipereka kwa inu.
Khalani mfumu mu mtima mwanga. Khululukirani chimo langa, ndipo
ndimupemphani kuti mudzaze moyo wanga ndi Mzimu wanu Woyera.
Zikomo Ambuye, ndikhulupirira kuti munandikhululukira tchimo
langa ndipo munandidzazadi ndi Mzimu Woyera, monga munalonjeza m Mawu
anu."
Amen
M'mene mungadziwire kuti
mwadzazidwa ndi Mzimu Woyera.
Mulungu alamulilra kuti tidzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo alonjeza
kuti adzatinvera tikapempha kalikonse kokomera Iye. Munapempha
chimene analamulira. kodi mudziwa kuti mwalandira?.
Khulupirirani Mulungu, zina zibwera m,mbuyo
Chitunzi ichi cha stima chitifanizira momwe ife tingathe
kudzazidwa ndi Mzimu Woyera mwakukhulupirira malonjezo a Mulungu.

- Mutu wa sitima ufanizira mphavu ili ndi Mulungu ndi Mau ace.
- Mwachikhulupiriro tilumikizidwa ku mphavu, imeneyo.
- Zina zotsimikizira kuti tapulumutsidwa, zibwera pambuyo.
Umo mukhoza kukhalabe wodzala ndi
Mzimu Woyera.
Mkristu angathe kukhala ndi moyo wodzala ndi Mzimu pokhapokha pamene
iye akhulupilira Mulungu.
Pamene Mzimu Woyera atsogolera ndi kulamulira moyo wanu:
- Zipatso za Mzimu Woyera zidzachulukilabe m'moyo wanu (Agalatiya
5:22,23).
- Mapemphero anu adzakhala ndi mpamvu (Yakobo 5:16)
- Kudzindikira kwanu kwa Mua a Mulungu kudzaonjezeka tsiku ndi tsiku
(2 Timoteo 3:16).
- Mudzalandira mphamvu yakuchitira Yesu umboni (Machitidwe 1:8)..
- Mudzakhala ndi mphamvu yogonjetsa nayo tchimo ndi mayesero a
Satana (1 Akorinto 10:13)
Kupuma mu Uzimu
Mukachimwanso mwa kulanda mpando wachifumu kuti mulamulire moyo
wanu, muyenera kuchita zinthu ziwiri izi:
- Lapani pa maso pa Mulungu pakuti mukachimwa mwa kuchita
chifuniro chanu kusanvera Iye. Mukatero Iye
zdzakukhulukirani ndi kukuyeretsaninso (1 Yohane 1:9).
- Dziperekeni kwa Yesu Kristu kuti iye alamulire moyo wanu
wonse (Aroma 6:13).
Khulupilirani Mulungu kuti Iye adzakudzazaninso ndi Mzimu Woyera.
Kumbukirani pa Aefenso 5:18 Iye alamulila kuti mudzazidwe ndi
Mzimu Woyera. Ndipo pa 1 Yohane 5:14,15, alonjeza kuti Iye
amatimvera tikapempha kanthu kalikonse komkomera Iye.
muchite zinthu izi ziwiri; kulapa ndi kulandira chikhululukiro pa
nthawi iliyonse pamene Mzimu Woyera akusonyezani kuti munachimwa.
Mukatero mudzakhala ndi moyo weniweni wosefukira nthawi zonse (Yohane
10:10).
Zimene mwalandira, gawani kwa Munthu wina.
Anthu ambirir-mbiri akhala nalo danga yowerenga aka kabuku "Kodi
munapeza Moyo weni-weni wa Uzimu". Aka kabuku kapezeka
mumalankhulidwe yosiyna-sina pa dziko lonse lapansi. Pamene Mkristu
apeza moyo weni-weni wa mu Uzmui, panenepo akhala ndi mphamvu mu
moyo wace. Ngati iye alola Mzimu Woyera kuti umulamulile
agonjetsa chimo, apewa zoipa ndipo amvera Mau a Mulungu.
Ngati mufuna kugula zomwe mwawerenga, munghate
kugula lelo. |
|